Mawu a M'munsi
a M’chaka cha 1922, ku Libya kunatentha kwambiri mpaka madigiri seshasi 58, ndipo mpaka pano sipanapezekeponso malo ena alionse pa dziko lonse lapansi amene anatenthapo kupitirira pamenepa. Komano, kutengera madigiri onse a m’nyengo yotentha, ku chigwa cha Death Valley n’kumene kumatentha kwambiri padziko lonse lapansi.