Mawu a M'munsi
b Ngakhale kuti anthu amene tawatchula mu nkhani ino ndi amuna, akazi ambiri amavutikanso ndi chizolowezi chodziseweretsa maliseche. Choncho malangizo amene aperekedwawa akukhudza amuna ndi akazi omwe. Onaninso kuti nkhani ino ikunena za kudziseweretsa wekha maliseche. Kuseweretsa maliseche a munthu amene simuli naye pabanja ndi mbali imodzi ya zimene Baibulo limatcha dama, lomwe ndi tchimo lalikulu kwambiri pamaso pa Mulungu.—Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Pali Cholakwika Kugonana Tisanakwatirane?” mu Galamukani! ya August 8, 2004, tsamba 12 mpaka 14.