Mawu a M'munsi
b N’zoona kuti Baibulo la Chigiriki la Septuagint n’limene ankaligwiritsa ntchito pogwira mawu a m’Malemba Achiheberi m’mbali ya Baibulo imene imatchedwa Chipangano Chatsopano. Popeza Mabaibulo a Septuagint olembedwa chaposachedwa alibe dzina la Mulungu, akatswiri ambiri amanena kuti dzinali liyeneranso kuchotsedwa m’Malemba Achigiriki Achikhristu. Komabe, Mabaibulo akale kwambiri a Septuagint amene alipobe ali ndi dzina lakuti Yehova, lolembedwa mmene ankalilembera kale m’Chiheberi. Zimenezi zikutipatsa mphamvu yobwezeretsa dzina la Yehova m’Malemba Achigiriki.