Mawu a M'munsi
b Al-Khwārizmī anali katswiri wotchuka wa masamu ku Persia, m’zaka za m’ma 800, ndipo iyeyu ndiye anayambitsa masamu otchedwa ajebra, ndi njira za ku India zowerengetsera masamu, monga kulemba manambala ndi zilembo monga 1, 2, 3, . . . ndiponso anayambitsa nzeru zogwiritsa ntchito ziro powerengera masamu. Iyeyu ndiye anayambitsa mfundo zikuluzikulu zogwiritsidwa ntchito pamasamu. Mawu akuti “algorithm,” ogwiritsidwa ntchito pamasamu, anachokera padzina lake.