Mawu a M'munsi
b Nyama zambiri zimatha kusiyanitsa mitundu, ngakhale kuti zimaona mitunduyo mosiyana ndi mmene ife timaonera. Mwachitsanzo, agalu ali ndi magulu awiri okha a maselo ozindikira mitundu m’maso mwawo. Ali ndi gulu lozindikira mtundu wabluu ndiponso gulu lina lozindikira mtundu wa pakati pa kufiira ndi kubiriwira. Koma mbalame zina, zili ndi magulu anayi a maselo ozindikira mitundu ndipo zingathe kuzindikira mitundu ya kuwala imene anthu satha kuzindikira.