Mawu a M'munsi
a Pali mitundu iwiri ya njati za ku Ulaya, ndipo mitunduyi ndi njati za m’zigwa ndiponso njati za ku Caucasia, kapena kuti za m’mapiri. Njati yomaliza ya ku Caucasia inafa mu 1927. Koma m’mbuyomo, njati ina yamphongo yamtundu umenewu anaiika pamodzi ndi njati yaikazi ya m’zigwa, ndipo panabadwa mwana wosakanikirana mtundu. Njati zosakanikirana mtundu za ku Caucasia zimenezi zidakalipo ndithu.