Mawu a M'munsi
a M’Malemba Achigiriki Achikhristu, kapena kuti “Chipangano Chatsopano,” pafupifupi malo onse pamene pamapezeka mawu akuti “chikondi,” amachokera ku mawu Achigiriki akuti agape. Chikondi cha agape ndi chikondi chimene munthu amasonyeza potsatira mfundo za makhalidwe abwino, kaya munthuyo akufuna kapena sakufuna, podziwa kuti ndi udindo wake kuchitira ena zabwino. Ndipo chikondi cha agape si chachinyengo koma n’chenicheni ndipo chimachokera mumtima.—1 Petulo 1:22.