Mawu a M'munsi
a M’pemphero la Ambuye, Yesu sananene kuti: “Choncho inu muzipemphera pemphero ili,” zimene zikanatsutsana ndi zomwe anali atangonena kumene. M’malo mwake iye anati: “Choncho inu muzipemphera motere.” (Mateyo 6:9-13) Kodi ankafuna kutiphunzitsa chiyani pamenepa? Malinga ndi zimene pemphero la Ambuye likusonyeza, tikamapemphera tiyenera kuganizira kwambiri zinthu zauzimu kuposa zofunika pamoyo wathu.