Mawu a M'munsi
a Chilengedwe chonsechi kuti chikhalepo m’pofunika mphamvu za mitundu inayi zimene zimagwira ntchito pa zinthu zonse za m’chilengedwe. Zina mwa mphamvu zimenezi zimakoka zinthu, zina zimakankha, ndipo zina zimatulutsa mphamvu yangati yamagetsi. Mphamvu zonsezi zimagwira ntchito mogwirizana, iliyonse pamlingo woyenera.—Onani mutu 2 wa buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.