Mawu a M'munsi
a Sikuti anthu onse angawasinthire mankhwala ngati mmene zinakhalira ndi Myra. Mwachitsanzo, anthu ena akadwala matenda opweteka kwambiri, amatha kupatsidwa mankhwala amphamvu omwe angathe kuwalowerera. Mankhwalawa amawamwa dokotala akuwayang’anira. Apa sitinganene kuti anthu oterewa akugwiritsa ntchito mankhwala molakwika.—Onani Miyambo 31:6.