Mawu a M'munsi
a Monga mmene zinalili mu nthawi ya atumwi, Akhristu enanso okhulupirika masiku ano ndi olemera. Komabe, Mulungu amawachenjeza Akhristu amenewa kuti asamadalire kwambiri chuma chawocho kapena kulola kuti chiwasokoneze. (Miyambo 11:28; Maliko 10:25; Chivumbulutso 3:17) Anthu onse amafunika kuika maganizo awo onse pakuchita chifuniro cha Mulungu, kaya akhale olemera kapena osauka.—Luka 12:31.