Mawu a M'munsi
a Zilembo zinayi zimenezi ndi makonsonanti okhaokha, ndipo amaziwerenga kuchokera kumanja kupita kumanzere. Zimathanso kulembedwa chonchi YHWH kapena chonchi JHVH. Kale, anthu akamawerenga zilembo zimenezi ankaikamo mavawelo, ngati mmene anthu amachitira masiku ano akamawerenga zilembo zoimira dzina linalake.