Mawu a M'munsi
b M’zinenero zoyambirira zimene Baibulo linalembedwa, dzina lenileni la Mulungu limapezeka koyamba palemba la Genesis 2:4. Dzinalo, lomwe limapezeka nthawi zoposa 7,000 m’zinenero zoyambirirazi, limatanthauza “Amachititsa Kukhala.” Ndipo zimenezi zimasonyeza kuti nthawi zonse Yehova amakwaniritsa zolinga zake. Chilichonse chimene wanena chimachitika.