Mawu a M'munsi
c Ngati ndinu a Mboni za Yehova ndipo mkazi wanu watsala pang’ono kuchira, mungachite bwino kudziwitsa Komiti Yolankhulana ndi Achipatala (HLC) ya kudera kwanu. Anthu a m’komiti imeneyi amayenda m’zipatala kuti athandize madokotala kusamalira odwala a Mboni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Komanso anthu a m’komiti imeneyi angathandize kupeza dokotala amene amalemekeza zimene wodwala amakhulupirira komanso amene amadziwa bwino kuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi.