Mawu a M'munsi
a Kuchita masewera olimbitsa thupi mopitiriza muyezo, mpaka kufika posiya kusamba ngati munthu ali wamkazi, kungachititse kuti mafupa akhale osalimba. Akuti ndi bwino kuti akazi a zaka zoposa 65 azikayezetsa mafupa awo kuchipatala kuti adziwe ngati mafupawo ayamba kufooka. Ngati mafupawo ayamba kufooka, akhoza kuwapatsa mankhwala kuti apewe kapena achiritse matendawa. Koma musanayambe kulandira chithandizo chilichonse, muyenera kuganizira kaye ubwino ndi kuipa kwake.