Mawu a M'munsi
a Ngakhale kuti pofika m’chaka cha 1854 ku London kunali zimbudzi zogejemula, njira yochotsera zoipa m’zimbudzizi inali yachikale. Zoipazi zinkayenda m’ngalande n’kukafika mumtsinje wa Thames, momwe munkachokera madzi amene anthu ambiri ankamwa.