Mawu a M'munsi
a Zaka zingapo m’mbuyomo, anthu ena ofufuza malo, Cunningham (mu 1828) ndi Leichhardt (mu 1843), anapeza mbewu ya mtedza wa makadamiya koma mbewuyo inangosungidwa osafufuzidwa bwinobwino. Mu 1857, mnzake wa Hill, dzina lake Ferdinand von Mueller, yemwe anali katswiri wa mbewu wa ku Melbourne, anapatsa mbewuyi dzina lakuti Makadamiya, pokumbukira mnzake wina wapamtima, dzina lake Dr. John Macadam.