Mawu a M'munsi
a Chikumbumtima cha anthu chimasiyana mogwirizana ndi chipembedzo chimene anakulira komanso kumvetsa kwawo zinthu zauzimu. Chofunika kwambiri n’chakuti munthuyo akhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu komanso asakhumudwitse chikumbumtima cha ena, kuphatikizapo cha anthu a m’banja lake. Lemba la Aroma 14:10, 12 limati: “Tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu wa Mulungu.”