Mawu a M'munsi
a Mwiniwake wa mahatchiwo amatha kusankha nthawi imene akufuna kuti hatchi yake ibereke. Hatchi imatha kubereka chaka ndi chaka, koma nthawi zina chaka chimatha osabereka. Mahatchi ambiri aakazi amakhala ndi moyo zaka 25 mpaka 30, ndipo pa nthawi imeneyi amatha kubereka ana 15 mpaka 18.