Mawu a M'munsi
c Posachedwapa, ofufuza apeza kuti molekyu ya RNA ndi yofunika kwambiri. Ngati RNA siikugwira bwino ntchito, munthu amatha kupezeka ndi matenda monga khansa, matenda enaake a pakhungu (psoriasis) ngakhalenso matenda oopsa kwambiri a mu ubongo (Alzheimer’s). Zimenezi zikusonyeza kuti mbali imeneyi, yomwe poyamba inkaoneka kuti ndi yopanda ntchito, ingathandize madokotala kudziwa matenda amene munthu akudwala komanso kuchiza matendawo.