Mawu a M'munsi
a Buku lina lolembedwa ndi D. H. Montgomery, linanena kuti m’chaka cha 1534, Nyumba ya Malamulo inavomereza kuti “mfumu Henry akhale mtsogoleri wa tchalitchi ku England, komanso munthu aliyense wotsutsana ndi zimenezi aziimbidwa mlandu woukira boma. Mfumuyi itangosaina lamuloli, ulamuliro wa apapa womwe unkayendetsa tchalitchi cha ku England kwa zaka zambiri unatha ntchito ndipo tchalitchi cha ku England chinakhala chodziimira pachokha.”