Mawu a M'munsi
a Zikuoneka kuti maganizo amenewa anawayambitsa ndi bishopu Isidore wa ku Seville, ku Spain (yemwe anabadwa mu 560 n’kumwalira mu 636 C.E.). Bishopuyu ananena kuti: “Pali zilankhulo zitatu zopatulika izi: Chiheberi, Chigiriki, ndi Chilatini. Ndipo zilankhulo zimenezi n’zapamwamba kuposa zilankhulo zonse padzikoli, chifukwa mlandu wa Ambuye unalembedwa pamtanda ndi Pilato m’zilankhulo zitatu zimenezi.” Koma mfundo imeneyi si yomveka chifukwa si Mulungu amene analamula kuti mlanduwo ulembedwe m’zilankhulo zimenezi.