Mawu a M'munsi
b Chifukwa chakuti nkhondo zambiri zikuluzikulu zinkachitikira m’dera limeneli, mawu akuti “Megido” anayamba kugwiritsidwa ntchito ponena za nkhondo yodziwika bwino kwambiri ya Aramagedo, yomwe m’Chiheberi amati Har–Magedon. Baibulo likamanena za Aramagedo limatanthauza nkhondo ya “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 16:14, 16.