Mawu a M'munsi
f Yesu “sanachite tchimo” ndipo chifukwa cha zimenezi sankayenera kufa. (1 Petulo 2:22) Komabe anapereka moyo wake kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa. N’chifukwa chake imfa ya Yesu imatchedwa nsembe ya “dipo.” (Mateyu 20:28) Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lomwenso limapezeka pa Webusaiti ya www.pr418.com.