Mawu a M'munsi
c Nthawi zambiri munthu akamadzivulaza amakhala kuti akuvutika maganizo kapena ali ndi matenda enaake. Choncho, angafunike kupita kuchipatala. Magazini ya Galamukani! simasankhira anthu zochita pa nkhani ya mankhwala. Komabe, Akhristu ayenera kuonetsetsa kuti thandizo lililonse lomwe angapeze lisakhale losemphana ndi mfundo za m’Baibulo.