Mawu a M'munsi
b Akatswiri a sayansi ya zinthu zakuthambo a ku Greece ndi amene anali oyamba kuchita zimenezi. Akatswiri a maphunziro achisilamu ankagwiritsa ntchito njirayi pofuna kudziwa kumene kuli mzinda wa Mecca womwe ndi wofunika kwambiri m’chipembedzo chachisilamu. Masiku anonso, Asilamu amayang’ana komwe kuli mzinda wa Mecca akamapemphera ndiponso akamazinga nyama. Komanso akamaika maliro, amawayang’anitsa komwe kuli mzindawu.