Mawu a M'munsi
a Si bwino kuchotsa mimba chifukwa choti dokotala wakuuzani kuti moyo wa mayi kapena wa mwana ukhoza kukhala pa ngozi. Koma ngati pa nthawi yobereka mayi ndi bambo auzidwa kuti ayenera kusankha pakati pa kupulumutsa moyo wa mayi kapena wa mwana, iwo ayenera kusankha okha zochita. Komabe masiku ano zimenezi sizichitikachitika mâmayiko ena chifukwa choti zipatala zawo zili ndi zipangizo zamakono.