Mawu a M'munsi
a M’mabaibulo ambiri anachotsamo dzina la Mulungu ndipo m’malomwake anaikamo dzina laudindo lakuti “AMBUYE” lolembedwa ndi zilembo zazikulu. Pomwe m’mabaibulo ena dzina la Mulungu anangolilemba m’mavesi owerengeka kapena m’mawu a m’munsi okha. Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika dzina la Mulungu limapezeka pafupifupi m’mabuku onse.