Mawu a M'munsi
a Mwachitsanzo, Baibulo limanena za nkhope ya Mulungu, maso ake, makutu ake, mphuno yake, pakamwa pake, mkono wake ndi mapazi ake. (Salimo 18:15; 27:8; 44:3; Yesaya 60:13; Mateyu 4:4; 1 Petulo 3:12) Sitiyenera kuganiza kuti mawu ophiphiritsa amenewa akusonyeza kuti Yehova alidi ndi ziwalo zimenezi, monganso mmene zilili ndi mawu amene amanena kuti iye ndi “Thanthwe” kapena “chishango.”—Deuteronomo 32:4; Salimo 84:11.