Mawu a M'munsi
a Zimenezi sizikusonyeza kuti munthu aliyense amene amakutsutsani akutsogoleredwa ndi Satana. Koma Satana ndi amene ali mulungu wa nthawi inoyo ndipo dziko lonse lapansi lili m’manja mwake. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Choncho, n’zochita kudziwikiratu kuti anthu ambiri sangakonde kutsatira malamulo a Mulungu ndipo ena angamakutsutseni pamene mukutsatira malamulowo.