Mawu a M'munsi
a Kuchokera mu 455 B.C.E. kufika mu 1 B.C.E panadutsa zaka 454. Kuchokera mu 1 B.C.E. kufika 1 C.E. panali chaka chimodzi chokha. Ndipo kuchokera mu 1 C.E. kufika mu 29 C.E. panadutsa zaka 28. Tikaphatikizira, zaka zimenezi zikukwana zaka 483. Yesu ‘anaphedwa’ m’chaka cha 33 C.E., womwe ndi mlungu wa 70. (Danieli 9:24, 26) Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! Mutu 11, ndi Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 231-233. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.