Mawu a M'munsi
a M’Malemba Achiheberi mulibe mawu enieni akuti “chikumbumtima.” Komabe, chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti anthu ankagwiritsa ntchito chikumbumtima. Mawu akuti “mtima” nthawi zambiri amanena za munthu wamkati. M’nkhani ya Yobu, zikuoneka kuti mawuwa akutchula za munthu wamkati, chomwe ndi chikumbumtima. M’Malemba Achigiriki Achikhristu, mawu Achigiriki otanthauza “chikumbumtima” amapezeka pafupifupi malo 30.