Mawu a M'munsi
b Baibulo limasonyeza kuti, ngati munthu chikumbumtima chake sichikumutsutsa, sizitanthauza kuti basi zonse zili bwino. Mwachitsanzo, Paulo anati: “Sindikudziwa kanthu kalikonse konditsutsa mumtima mwanga. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, koma Yehova ndiye amandifufuza.” (1 Akorinto 4:4) Ngakhale anthu amene amazunza Akhristu, monga mmene Paulo ankachitira asanakhale Mkhristu, angazunze Akhristu popanda kutsutsidwa ndi chikumbumtima chawo chifukwa choganiza kuti akuchita zimene Mulungu amakondwera nazo. Choncho, chofunika kwambiri sikungokhala ndi chikumbumtima chosatitsutsa, koma chiyeneranso kukhala choyera pamaso pa Mulungu.—Machitidwe 23:1; 2 Timoteyo 1:3.