Mawu a M'munsi
a Kuyambira pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Khristu wakhala akulamulira mpingo wa otsatira ake odzozedwa wapadziko lapansi pano monga Mfumu. (Akolose 1:13) Kenako mu 1914, Khristu analandira ulamuliro ndipo ali ndi mphamvu pa “ufumu wa dziko.” Choncho, Akhristu odzozedwa ndi akazembe a Ufumu wa Mesiya.—Chivumbulutso 11:15.