Mawu a M'munsi
a Pofuna kupewa kugwiritsa ntchito kompyuta molakwika, mabanja ambiri amaiika pamalo oonekera. Komanso ena amagula mapulogalamu otetezera kuti zinthu zosayenera zisalowe mu kompyuta yawo. Komabe, palibe pulogalamu imene ingatetezeretu kompyuta yanu ku zinthu zosayenera.