Mawu a M'munsi
a Ayuda ena ankadana ndi anthu ofufuta zikopa chifukwa ntchitoyi inkawachititsa kuti azigwira zikopa, nyama zakufa komanso ankagwiritsa ntchito zinthu zina zonyansa pogwira ntchitoyi. Anthu ofufuta zikopa ankaonedwa kuti ndi osayenera kufika pakachisi, ndipo malo awo ogwirira ntchito ankafunika kukhala kunja kwa mzinda pa mtunda pafupifupi mamita 20. Mwina chimenechi chinali chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti nyumba ya Simoni ikhale “m’mbali mwa nyanja.”—Mac. 10:6.