Mawu a M'munsi
g Kuyambira pamenepa, Saulo anayamba kutchedwa kuti Paulo. Ena amanena kuti Saulo anasankha dzina la Chiroma limeneli popereka ulemu kwa Serigio Paulo. Komabe, Saulo anapitiriza kugwiritsa ntchito dzina lakuti Paulo ngakhale atachoka ku Kupuro, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti Paulo, amene anali “mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina,” anaganiza zosintha dzina lakeli kuti azidziwika ndi dzina la Chiroma. Iye ayenera kuti anasankha dzina lakuti Paulo chifukwa chakuti katchulidwe ka dzina la Chiheberi lakuti Saulo, m’Chigiriki kamafanana ndi katchulidwe ka mawu ena otukwana.—Aroma 11:13.