Mawu a M'munsi
b Pulofesa Shapiro sakhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Amakhulupirira kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi m’njira inayake yomwe panopa sitikuidziwa bwinobwino. Mu 2009, asayansi a pa yunivesite ya Manchester ku England ananena kuti anakwanitsa kupanga mamolekyu enaake otchedwa manyukiliyotaidi. Komabe, Shapiro ananena kuti zinthu zimene anagwiritsa ntchito popanga mamolekyu amenewa sizikugwirizana ndi zinthu zimene iyeyo akudziwa kuti zimapanga RNA.