Mawu a M'munsi
a N’zochititsa chidwi kuti Rute sanangotchula kuti “Mulungu” ngati mmene anthu amene sankalambira Yehova ankachitira. M’malomwake iye anagwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova. Baibulo lina linanena kuti: “Pamenepa amene analemba buku la Rute anatsindika mfundo yoti, ngakhale kuti Rute sanali Mwisiraeli, ankalambira Mulungu woona.”—The Interpreter’s Bible.