Mawu a M'munsi
a Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Yehova “anali atatseka mimba” ya Hana, palibe umboni wosonyeza kuti Mulungu sankasangalala ndi Hana, yemwe anali mkazi wokhulupirika komanso wodzichepetsa. (1 Sam. 1:5) Nthawi zina Baibulo limanena kuti Mulungu wachita chinachake, koma kwenikweni amakhala kuti wangolola kuti chichitike.