Mawu a M'munsi
b Nthawi zambiri phiri la Karimeli limakhala lobiriwira komanso kumawomba kamphepo kayeziyezi kochokera m’nyanja. Zimenezi zimachititsa kuti kuzigwa mvula kawirikawiri komanso kuzikhala mame ambiri. Anthu olambira Baala ayenera kuti ankaona kuti phiri limeneli ndi malo ofunika kwambiri, chifukwa ankakhulupirira kuti Baala ndi amene amabweretsa mvula. Koma pa nthawiyi zinasonyezeratu kuti Baala ndi mulungu wonyenga chifukwa phiri la Karimeli linali litauma ndiponso linali lopanda zomera.