Mawu a M'munsi
d Hamani analonjeza kupereka matalente 10,000 asiliva ndipo masiku ano ndalama zimenezi ndi zokwana madola mamiliyoni ambiri. Ngati Ahasiwero analidi Sasita Woyamba, ndiye kuti anakopeka kwambiri ndi ndalama zimene Hamani analonjezazi. Sasita ankafunikira ndalama zambiri zoti agwiritse ntchito pa nkhondo yomenyana ndi Agiriki, yomwe pamapeto pake analuza.