Mawu a M'munsi
e Sasita Woyamba ankadziwika kuti anali munthu wosachedwa kupsa mtima. Mwachitsanzo, katswiri wina wa ku Greece wolemba mbiri yakale, dzina lake Herodotus, analemba zinthu zina zimene Sasita anachita pamene ankamenyana ndi Agiriki. Mfumuyi inalamula kuti panyanja ya Hellespont pamangidwe mlatho pogundaniza mabwato. Mphepo yamkuntho itaphwasula mlathowo, Sasita analamula kuti anthu amene anamanga mlathowo adulidwe mitu. Analamulanso asilikali ake kuti alange nyanjayo mwa kukwapula madzi kwinaku akuwerenga mokweza mawu olalata. Pa nkhondo yomweyi, munthu wina wolemera atapempha kuti mwana wake asalowe usilikali, Sasita analamula kuti mwanayo adulidwe pakati ndipo mtembo wake uikidwe poonekera kuti anthu ena atengerepo phunziro.