Mawu a M'munsi
b Lameki anapatsa mwana wake dzina loti Nowa lomwe limatanthauza “Mpumulo” kapena “Chitonthozo.” Iye analoseranso kuti Nowa adzakwaniritsa tanthauzo la dzina lake pothandiza kuti temberero la nthaka lichotsedwe. (Gen. 5:28, 29) Koma Lameki anamwalira ulosi umenewu usanakwaniritsidwe. N’kutheka kuti mayi ake a Nowa, azichimwene ake komanso azichemwali ake anafa ndi Chigumula.