Mawu a M'munsi
c Dzina lakuti “Satana” limagwiritsidwa ntchito ponena za munthu maulendo 18 m’Malemba Achiheberi. Koma m’Malemba Achigiriki mawu akuti “Satana” amapezeka maulendo oposa 30. Zimenezi zinali zoyenera chifukwa Malemba Achiheberi sankafunikira kufotokoza kwambiri za Satana koma kufotokoza mfundo zomwe zingathandize anthu kuzindikira Mesiya. Mesiya atabwera anathandiza anthu kumudziwa Satana ndipo zimenezi zinalembedwa m’Malemba Achigiriki.