Mawu a M'munsi
a M’chaka cha 1932, Buku Lachiwiri la Vindication linafotokoza koyamba kuti ulosi wa m’Baibulo wonena za kubwezeretsa anthu a Mulungu kudziko lawo ukukwaniritsidwanso masiku ano, osati pa Aisiraeli akuthupi koma pa Isiraeli wauzimu. Maulosi amenewa ankanena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1999, inafotokoza kuti masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona unali ulosi wonena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera ndipo kukwaniritsidwa kwake kwenikweni kukuchitika masiku otsiriza ano.