Mawu a M'munsi
a Ayuda ambiri amene anali ku ukapolo ankakhala m’midzi imene inali kutali ndi mzinda wa Babulo. Mwachitsanzo, Ezekieli ankakhala limodzi ndi Ayuda amene ankakhala pafupi ndi mtsinje wa Kebara. (Ezek. 3:15) Koma panalinso Ayuda ena ochepa amene ankakhala mumzinda. Pa gulu la anthu amenewa panali “amʼbanja lachifumu komanso anthu olemekezeka.”—Dan. 1:3, 6; 2 Maf. 24:15.