Mawu a M'munsi
a Mayinawa ali ndi tanthauzo lapadera. Dzina lakuti Ohola limatanthauza “Tenti Yake [yolambirira.]”—mwina tanthauzo la dzinali likugwirizana ndi zimene Aisiraeli ankachita pokhazikitsa malo awo olambirira m’malo mopita kukachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Koma dzina lakuti Oholiba limatanthauza kuti “Tenti Yanga [yolambirira] Ili mwa Iye.” Ku Yerusalemu ndi kumene kunali nyumba yolambirira ya Yehova.