Mawu a M'munsi
a Yehova amafunitsitsa kuthandiza anthu amtima wosweka. (Salimo 34:18) Anthu oterewa amakhala ndi ululu waukulu mumtima mwawo moti amafuna kudzipha. Koma Yehova amawamvetsa ndipo amafunitsitsa kuwathandiza. Kuti muone mmene malangizo a m’Baibulo angathandizire munthu kuti asiye kuganiza zofuna kudzipha, werengani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” pagawo lakuti Onani Zinanso m’phunziroli.