Mawu a M'munsi
a Yohane pano anagwiritsira ntchito khaiʹro, komwe kunalinso kupatsa moni konga ngati “tikulandirani” kapena “tikuwoneni.” (Machitidwe 15:23; Mateyu 28:9) Iye sanagwiritsire ntchito a·spaʹzo·mai (monga mu versi 13), imene imatanthauza “kukumbatirana, mwakutero kupereka moni, kulonjera” ndipo chikanatanthauza kupatsa moni kotentha, ngakhale ndi kukupatirana. (Luka 10:4; 11:43; Machitidwe 20:1, 37; 1 Atesalonika 5:26) Chotero chitsogozo cha pa 2 Yohane 11 chikatanthauza bwino lomwe kusanena ngakhale “tikuwoneni” kwa oterewa.—Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1986, tsamba 30.